Bwererani ku Malo a Maphunziro
Ng’amba (El Niño) ya 2026/27: Zomwe Alimi a ku Malawi Akuyenera Kudziwa ndi Kuchita Panopa
Mvetserani nkhaniyi
Owerenga ndi Esther Mbewe 8:40

Zimene zatsimikizidwa pa 19 August 2026
NOAA ndi bungwe la boma la United States lotchedwa National Oceanic and Atmospheric Administration. Gawo lake la Climate Prediction Center limayang’ana nyanja ya Pacific ndi mlengalenga kuti lidziwe El Niño ndi mmene ingakhalire. Chidziwitso cha NOAA cha 13 August 2026 chikuti El Niño ikukulirakulira ndipo ili ndi mwayi woposa 90 pa 100 wokhala yamphamvu kwambiri m’nyengo ya 2026/27.
Mlimi wa ku Malawi ayenera kudziwa zimenezi chifukwa NOAA imapereka chenjezo loyambirira lakuti zoopsa za nyengo zingasinthe. Koma uthenga wake wa padziko lonse supereka tsiku lobzala kapena kuchuluka kwa mvula m’dziko la Malawi.
DCCMS ndi Dipatimenti ya Kusintha kwa Nyengo ndi Ntchito za Nyengo ya boma la Malawi. Ntchito yake ndi kuyang’anira nyengo ya m’dziko muno ndi kupereka zanyengo nthawi zonse, za m’maboma komanso za masiku ochepa. Kwa mlimi wa ku Malawi, uthenga wa DCCMS ndiwo wofunika kwambiri chifukwa umakhudza nyengo ya kuno ndipo umasinthidwa pafupipafupi. Onani zanyengo zaposachedwa za DCCMS komanso uthenga wa nyengo wa masiku khumi, ndipo onetsetsani tsiku limene uthengawo unatulutsidwa. Uthenga watsopano ukatuluka, gwiritsani ntchito watsopanowo osati wakale.
Zinthu zitatu zoti mudziwe musanabzale chimanga
- Onani zanyengo zovomerezeka za dera lanu. Uthenga wa El Niño wa padziko lonse sukufotokoza mwachindunji mmene nyengo idzakhalire m’dera lanu.
-
Onani chinyezi pofukula nthaka. Mvula ikagwa, kumbani malo angapo kuti muone ngati nthaka yanyowa mpaka pansi, osati pamwamba pokha.
- Onani zanyengo za masiku khumi otsatira. Gwiritsani ntchito zanyengo zaposachedwa komanso malangizo a alangizi a zaulimi musanadzale kapena kugwira ntchito yaikulu ya m’munda.
Palibe tsiku limodzi lokhazikika lobzala lomwe lingagwire ntchito pa minda yonse. Werengani malangizo a kubzala chimanga ndi mipata.
Konzani Munda Mwanzeru Ngakhale Ng’amba Isanatsimikizike
Konzani makhwawa, mabeseni kapena ngalande molingana ndi nthaka ndi potsetsereka. Sungani madzi amvula ofunika, koma tulutsani ochuluka. Zotsalira za mbewu (mapesi) zopanda matenda zigwiritseni ntchito ngati chophimba ngati alangizi avomereza. Musaziwotche.

Gwiritsani ntchito kompositi wokhwima kapena manyowa oola bwino pamalo oyenera. Dziwani malo ofooka, amchenga, okokoloka kapena amene madzi amayima. Dongosolo la chonde cha nthaka la gawo ndi gawo likufotokoza chifukwa chake mbali zosiyanasiyana za munda zimafunika kusamalidwa mosiyanasiyana.
Sankhani Mbewu Mwanzeru
Sankhani mbewu yovomerezeka yomwe nthawi yake yokhwima ikugwirizana ndi dera lanu. Funsani wogulitsa kapena mlangizi kuti akufotokozereni zomwe zalembedwa pathumba. Mbewu yofulumira kukhwima kapena yopirira chilala ingachepetse chiopsezo, koma sikuti imatsimikizira zokolola.

Ngati muli ndi malo okwanira, chakudya chokwanira komanso anthu ogwira ntchito, ndi bwino kulima chimanga pamodzi ndi mtundu wa nyemba zoyenera kusiyana ndi kudalira mbewu imodzi yokha.
Konzani madzi, ziweto ndi feteleza pamodzi
Mvula ikachedwa kapena ikamagwa mosakhazikika, imakhudza madzi a pakhomo, chakudya cha ziweto komanso mapesi otsalira m’munda. Sungani madzi pamalo otetezeka ndipo konzani zomweramo ziweto. Sankhani mapesi abwino oti aphimbe nthaka, ndipo ena musunge ngati chakudya cha ziweto.

Musawonjezere kapena kuchepetsa feteleza chifukwa cha dzina la El Niño lokha. Mtundu, mlingo ndi nthawi zimadalirabe mbewu, nthaka, chinyezi ndi malangizo atsopano. Mukatsimikiza malangizo a dera lanu, werengani malangizo a malo oyenera kuthira feteleza wa chimanga.
Zinthu Zofunika Kuona Musanapange Chisankho cha pa Sabata lirilonse
- Lembani zanyengo, kumene mwazitenga ndi tsiku limene zatulutsidwa.
- Lembani mvula yomwe yagwa ndi kuya kwa chinyezi m’malo angapo.
- Lembani mtundu wa mbewu, nthawi yakukhwima ndi dera limene ikuyenerera.
- Lembani vuto lenileni la gawo la munda: madzi othamanga, kuuma msanga kapena madzi oima.
Zisankho zimene mlimi angakumane nazo
Kodi El Niño ikutanthauza kuti minda yonse ku Malawi idzakhala ndi chilala kapena ng’amba? Ayi. El Niño imawonjezera chiopsezo cha mvula yanjomba, ng’amba kapena kuti chilala, koma sizitanthauza kuti madera onse adzakhudzidwa mofanana. Choncho, pokonza ulimi wanu, tsatirani zanyengo za Malawi komanso za dera lanu.
Kodi ndibzale mvula yoyamba ikagwa? Yambani ndi kuyang’ana chinyezi pansi pa nthaka ni chidziwitso chatsopano cha masiku khumi .
Kodi ndigule feteleza wowonjezera panopa? Osagula chifukwa chongomva za El Niño. Choyamba ganizirani kukula kwa munda, mbeu imene mubzale, mtundu ndi mlingo wa feteleza, nthaka, chinyezi komanso malangizo a alangizi.
Magwero a nkhaniyi anatsimikizidwa pa 20 August 2026. Zanyengo zimasintha, choncho musanapange chisankho pa ulimi wanu, onaninso uthenga waposachedwa wa NOAA wokhudza El Niño komanso wa DCCMS wokhudza nyengo ya ku Malawi.